08/02/18

Written by  Newsroom

Mkulu wina wa udindo wake ku chipembedzo china kwa mfumu Maliri m’boma la Lilongwe waba ndalama za mpingo, njinga ya mkulu amene amayang’anira mpingowu mderali komanso mikanjo yomwe amavala akamapempheretsa.

08
February

Mkuluyo atabwera anauza mzakeyo kuti akufuna mbeta. Winayo sanakaike ndipo anamupezera mbetayo ndipo anagwirizana zomanga banja. Zinthu zimayenda ndipo chomwe amadikira ndi choti achibale a mbali ziwirizi akumane, adziwane ndipo amange chinkhoswe. Koma mkulu uja ananyengerera mtsikana uja kuti adzigona naye. Pofuna kusakhumudwitsa njondayo, amazemberana. Patatsala tsiku limodzi kuti abale ake a mwamuna akakumane ndi akuchikazi, mkulu wapa mpingo uja anadzidzimuka kuti njinga yake yasowa. atafufuza, anatulukiranso zoti mikanjo yake komanso ndalama zapa mpingowo zasowa. Atapita ku chipinda komwe amagona mkulu-yo anapeza kuli pululu iye kulibe. Anayetsera kumuimbira foni koma siinagwire mpaka kunada. Mamawa, mkulu wapa mpingoyo anapita kwa makolo a mtsikana uja kukafotokoza za nkhaniyi. Kumeneko anamuuza kuti akamabwerera kwao, amutenga mtsikanayo chifukwa ali ndi pakati pa mzakeyo. Panopa banjalo langoti kakasi ndi zimenezi.



Mwambi uja woti Woipa athawa yekha wapherezera m’boma la Phalombe. Banja lina ku Naminjiwa m’boma la Phalombe lathawa mderalo kusiya nyumba, litadziwa zoti mwini katundu amene bambo wa mnyumbamo anakaba m’dziko la Mozambique, wadziwa zoti katundu wakeyo amubitsa pa dzenje mnyumbamo. Bamboyo ataba katunduyo anafika naye ku nyumba ndipo anakumba dzenje mnyumbamo mkubitsa katunduyo. Tsiku lina bambo wakubayo anadzidzimuka atamva mwini katunduyo akunena zoti katundu wake amubitsa mdzenje lomwe mnyumba ina mderalo ndipo akubwerera kaye kwao ku Mozambique, katunduyo adzatengabe. Mkuluyo anayamba kupumira m’mwamba ndipo atafika ku nyumba anauza banja lake kuti mwini katunduyu wadziwa zoti katundu wake anamubitsa pa dzenje mnyumbamo. Apa mbanjalo silinasinkhe-sinkhe zochita, koma mwansangansa kukhoma nyumbayo, nkusiya katundu yemwe anabayo pa dzenje pomwepo nkubaduka kotero kuti m’mene timalandira nkhaniyi anthu mderalo sakudziwa komwe banjalo lathawira.


Mai wina kwa mfumu Nkhumba m’boma la Mulanje akusowa mtengo wogwira amuna awiri amene anagwirizana zomanga nawo banja atamusasa nthawi imodzi. Maiyo anakwatiwa ndi mwamuna wa mdera la kwao lomwelo ndipo patatha zaka banjalo linatha. Miezi yapitayi, maiyo anakacheza kwa m’bale ake ku Chiradzulu, komwe anakumana ndi mwamuna amene anamvana zomanga banja. Mwamuna anatengana ndi mkaziyo kupita kwao kwa mkazi-yo kuti akadziweko. Patatha masiku ochepa, analawira mkaziyo kuti akukatenga a malume ake kuti adzamange unkhoswe. Atangochoka, mkaziyo anakumana ndi mwamuna wake wakale uja nkugwirizana zoti abwererane. Izi zinathekadi chifukwa m’mene mwamuna watsopano-yo amafika pakhomopo ndi abale ake, anapeza kulibe mkaziyo. Abale a mkaziyo anamva zoti ali kwa mwamuna wake wakale ndipo atapita, anakamupezadi. Atamufunsa anagoti zolii. Abale ake a mwamuna wakaleyo sanatsangalale ndi zimenezi ndipo anauza m’bale wakeyo kuti ali pa dzuwa, amusiye mkaziyo chifukwa adzamuthawa monga momwe achitira ndi mwamuna wake watsopano-yoe. Akukambirana nkhani-yi anatulukira mwamuna watsopano uja ndi abale ake. Posakhalitsa amuna awiriwo anauza mkaziyo kuti ndi Hule ndipo onse limodzi anamusasa mogweirizana mkumusiya manja ali mkhosi.



Ndeu yosowa wolelesa inabuka pakati pa amai awiri, mkachisi wina ku Molele m’boma la Thyolo. Mwamuna wa maiyo ndi Chior Master gulu la Choir la mpingowo, ndiponso amayimba keyboard. Masiku apitawa, Choir Master-yo, anauza mtsikana wina wamu gululo kuti adzimuphunzitsa kuyimba keyboard-yo Mtsikanayo sanawiringule ndipo anayamba kuphunzitsana. koma nkhaniyi itamupeza mkazi wa Choir Master yo sanasangalale nayo. Atamufunsa mwamuna wake, sanayankhe zokhutiritsa ndipo ananyamuka nkupita kwa mtsikanayo nkukamuuza kuti aleke kuphunzitsana Keyboard-yo. Koma mtsikanayo anayankha motumbwa ndipo anatemetsa nkhwangwa pa mwala kuti sangaleke kuphunzira Keyboard-yo ndi Choir Master-yo. Tsiku lina, maiyo atapita kukachisiko mwadzidzidzi, komwe anapezerera anthu awiriwa atakolekerana miendo. Maiyo sanafunse ndipo anangofikira kuponya chibakhera kwa mtsikanayo yemwe anayamba kubwezera. Apatu ndeu yafumbi inabuka ndipo mwamunayo analephera kuleletsa kotero kuti anthu ena ndi amene anathandiza kuleletsa ndewu-yo. Panopa, amai awiriwa akuwonana ndi diso la nkhwezule.

Get Your Newsletter