14/01/18

Written by  Newsroom

Mtengwa wina mdera la Kacheche ku Mzimba ati sakumvetsa ndi zomwe zamuchitikira.

14
January

Nkhaniyi ikuti mwamuna wa mkaziyo anachoka mderalo kupita ku Joni kogwira ntchito ndipo apa maiyo anangoti laponda nkuyamba kuyenda ndi njonda zina. Mphekesera inamupeza mwamunayo ndipo wakhala akuuza abale komanso amzake kuti asadandaule ndi nkhaniyi zomwe zimadabwitsa anthuwo. Masiku apitawa mwamuna wa maiyo anatumiza foni ya m’manja yapamwamba ndiponso yamakomo kwa mkazi wake mcholinga choti adzigwiritsa ntchito. Koma posazindila za momwe imagwirira ntchito foniyo zonse zomwe akhala akulankhulana ndi zibwenzi zake zimajambulika ndikusungika mu foniyo. Mwadzidzidzi mwamuna wa maiyo anafika pa khomopo koma samaonetsa kukhumudwa ndipo naye mkaziyo anangoti kunja kulinji. Mwamunayo kenako anapempha mkazi wakeyo kuti amubwereke foniyo ndipo maiyo sanamukaikire kuti anali ndi zolinga zina. Mwamunayo anakwanitsa kupeza mauthenga onse ndipo apa anatengera foniyo kwa makolo a mbali ziwiri. Ku bwalo la milandu mwamuna wa chibwenzi komanso maiyo anasowa choyankhula chifukwa zonse zinali pa mbalambanda. Ku bwalolo mwa zina maiyo sanamvetse pa zomwe zinamuchitikira ndipo anayesetsa kupepesa koma sizinamveke ndipo banja lithathera pomwepo.

 

Mkamwini wina kwa Mkando ku Mulanje anamuonetsa nsana wa njira dzuwa likuswa mtengo. Nkhaniyi ikuti mwamunayo zaka zingapo zapitazo anadzakwatila mderalo ndipo zinthu zonse zimayenda bwino lomwe. Chaka chatha m’modzi mwa anthu apa banjapo anamwalira ndipo anasiya ana angapo. Chifukwa chokhazikika komanso kudzimva kwa mkamwiniyo kuti wakhazikika anayamba kuonesa manga ake pochita zinthu zosiyna-siyna zolakwika kuphatikizapo kulanda katundu wa ana amasiye. Pa chifukwachi anthu apa banjapo kuphatikizapo magulu ena okhudzidwa anayamba kulondola za nkhaniyi ndipo zinadziwika kuti mkamwiniyo anali olakwa. Apa anthuwo mogwirizana ndi akubanja anakasumila mkuluyo ndipo ku bwalo la milandu anangoti kukamwa yasa. Bwalolo kumapeto kwake anauza mkamwiniyo kuti achoke pakhomopo. Mwa katundu wina yemwe mkamwiniyo anatenga ndi monga njinga zakapalasa, ziwiya ndi zina. Mkamwiniyo anaona ngati kutulo m’bandakucha atamulonderela njira yakwao. Choseketsa mkamwiniyo amadzilankhulira yekha kuti akudandaula kuti wakula komanso kuti ati wasiya chuma chake.

 

Mwamuna wina mdera la Khonsolo ku Mzimba zamukoka manja atamugwira ali buno-buno ndi mdzukulu wake. Nkhaniyi ikutu mwamunayo mkazi wake anamwalira zaka zingapo zapitazo koma wakhala asakupeza banja chifukwa cha umbombo. Pa chifukwachi amakhala ndi achibale ambirimbiri kuphatikizapo adzukulu ake. Paja pali mau oti pafupi mpomwe wafika mwamunayo anayamba kuzemberana ndi mdzukulu wake ngakhale koyambilira mdzukuluyo amakana. Chibwenzicho chinafika pofumbila mpakana kutenganilana ku nyumba zogona alendo komanso kugulirana zinthu . Tsiku lina anawapezerela ali buno-buno koma nkhaniyi inafera m’mazila. Masiku apitawa mkuluyo anakabwereka ndalana ku gulu lomwe ali lobwereketsana komanso kukongozana ndalama mcholinga choti asangalatse mdzukulu wakeyo. Masiku obweza ndalamayo atafika mwamunayo zinamukoka manja chifukwa mwa ziuna bizinesi yomwe amayendetsa simayendanso ngati kale. Apa gulkulo sanaimve koma kulanda katundu osiyana-siyana kuphatikizapo wa mdzukulu wakeyo. Apa mdzukuluyo sanaimve koma kuulura za chibwenzi chake ndi malume akewo zomwe zinachititsa kuti gululo ligwire pakamwa. Pakadali pano nkhani ili mkamwamkamwa mderalo ndipo mwamunayo akuyenda zodula chifukwa cha nkhaniyi.

 

Mwambo olonga ufumu unasokonezeka mdera la Gulupu Nkutumura ku Ntcheu. Nkhaniyi ikuti mderalo munali chilinganizo cholonga ufumu ndipo pa mwa mwambo wake anthu omwe amayendetsa mwambowo anaitana gule wamkulu kuti akasangalatse anthu ndi mavinidwe ake a chikoka. Mwambowo utangoyamba kumene gule wamkuluyo analowa mbwalolo uku akulozera ndodo ya moto mbwalolo ati pofuna kudziumitsa thupi monga achitila pa mwambo wake, koma mwatsoka anatentha m’modzi mwa anthu omwe anali nawo pa mwambowo. Apa munthuyo pokhala kuti naye ndi katakwe wakudabwe anabweza moto potenthanso gule wamkuluyo. Apa gule wamkuluyo analiatsa liwiro ngati analibe mafupa kuthawira kudambwe. Mwambowo apa unasokonezeka chifukwa mwa zina anthu anaiwala za mwambowo koma kuseka mosalekeza. Malipoti ochokera ku dambwe ati gule wamkuluyo analira momvetsa chisoni uku akupempha thandizo komanso kunenetsa kuti wasiya kuvina gule. Anthu ena komanso mikoko yogona anadzudzula kwambiri munthu yemwe anatentha gule wamkuluyo pamene ena ati gule wamkuluyo sanasunge mwambo wakudambwe. Pakadali pano akuluakulu akudambwe ati akhalirana pansi kuti aone chomwe angachite ndi nkhaniyi mogwirizana ndi nyakwawa ya mderalo.

 

Get Your Newsletter