AKOMOKA NDI KACHASU KU MZIMBA Featured

Written by  Zam'maboma

Mnyamata wina m’dera la Mfumu Mabilabo mboma la Mzimba wabwelera lokumbakumba, atakomoka ndi kachasu.   

Nkhaniyi ikuti mnyamatayo ndi mbiya ng’ambe moti sizimatheka kukhala osamwa tsiku liri lonse.


Nthawi zambii mnyamatayo asanapite kokaledzera, amayamba waphika nsima nkudya koma pa tsikulo anangochoka m’mimba mulibe kanthu.

Atapapila kabangayo analedzera mopyola muyezo ndiye ndi kusadyako analenguka nawo mowawo mpaka anagwa pansi nkukomoka.  

Anthu ena atamuona anaphikitsa phala kwa mayi wina nkumukanula kukamwa kumumwetsa ndipo apo anaoneka ngati wapezako mphamvu.

Komabe anthuwo ataona kuti sizikuthandiza kwenikweni anamutengera ku chipatala komwe anakatsitsimuka.

Pakadali pano achibale a mnyamatayo amulangiza kuti asiye kumwa mowa mwauchidakwa pomwe anati akapitiliza khalidwe lakelo, tsiku lina adzakomoka koma sadzadzukanso.  


Zikuoneka kuti panopa mnyamatayo wadekha chifuwa kuyambira tsikulo sakupitanso kopapila mowawo pomwe akumauza anthu kuti  amalota anthu ena akumukokera m’dzenje.

Get Your Newsletter