CHAKWERA SALORA KUTI PULOGRAMU YA AIP ISOKONEZEDWE

Written by  MBC Online
Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera watsimikizira mtundu wa a Malawi kuti salora kuti pulogramu ya AIP yomwe inapereka mwayi kwa alimi mdziko muno kupeza zipangizo zaulimi zotsika mtengo isokonekere.
Alimi apindula ndi AIP chaka  chatha Alimi apindula ndi AIP chaka chatha
22
August
Mtsogoleriyu anayankhula izi kwa mtundu wa a Malawi mu mzinda wa Lilongwe dzulo pa August 21, kudzera pa wailesi za MBC.
 
Zomwe anayankhula Dr Chakwera zinali motere:
 
A Malawi anzanga, lero, ndikufuna timvetsetsane pa nkhani ya Affordable Inputs Programme (AIP). 
 
Tonse tikudziwa kuti pulogramu imeneyi ndi 
imene yatukula ulimi chaka chathachi; pulogramu  imene inabweretsa feteleza ndi zipangizo zina  zaulimi motchipa; pulogramu imene yadzadzitsa  nkhokwe za anthu ammidzi ndi chimanga cha  nkhani nkhani; pulogramu imene yathetsa njala 
muno m' Malawi. 
 
Koma lero tsogolo la pulogramu imeneyi 
likuwadetsa nkhawa alimi athu, ndiye ndimati  ndipereke chilimbikitso ndi chitsimikizo kwa nonse amene mumachita za ulimi. 
 
Chaka chatha munagula fetereza wotchipha, fetereza osafika K5,000, koma izi ena sizinawasangalatse. 
 
Ndiye pano akweza mtengo wafetereza mpaka kupyola. K30,000, ndi cholinga  choti akhaulitse inu alimi. 
 
Koma chomwe ndikufuna mudziwe ndi 
choti ine ndi Boma langa sitingasekelere zimenezo. 
 
Sitingasekelere zoti wina aphe ulimi mdziko 
muno. Wina afune asafune, alimi agula fetereza motchipa chaka chino. 
 
Ngakhale mtengo wake utakwere pang’ono 
chifukwa choti mitengo yafetereza yakwera dziko lonse lapansi, kukwera kwake sikukhala ngati komwe ogulitsa fetereza akuchita panoku. Zimenezo ine sindilora. 
 
 
Chachiwiri, sindilora kuti wina achotse dzina la banja lina lililonse olo mudzi wina uliwonse pa mndandanda wa omwe atagule fetereza wotchipayu. Zimenezonso ine ndiye 
ndikukanilatu.  Ngati pali anthu amene amasunga dziko lino, ndiye ndi alimi, ndipo ngati pali anthu amene ine ndinalumbila kuti ndidzawamenyera nkhondo, ndiye ndi alimi.
 
Yense amene akuchita zozunza alimi adziwe kuti akulimbana ndi Chakwera, ndipo 
saazikwanitsa. 
 
 
Zomwe boma langa litachite pa nkhani izi 
tilengeza masiku akubwerawa, koma lero 
ndimafuna ndineneretu kuti pulogramu ya AIP sindilora kuti  iwonongedwe. 
 
 
Zikomo
 
#MBCNewsLive
 

Get Your Newsletter