WATENGA PATHUPI MWAMUNA WAKE ALI KU JONI Featured

Written by  Zam'maboma

M’dera la Mfumu Wimbe mboma la Kasungu, mkulu wina yemwe anasiya mkazi wake kuno kumudzi kupita ku joni kukazisaka, wakhumudwa kwambili atamva kuti mkazi wakeyo ali ndi pathupi.  


Nkhaniyi ikuti mkuluyo anapita ku joniko zaka zingapo zapitazi ndipo akuti amamutumizira mkaziyo ndalama zokwana mwezi uli onse.

M’malo moyamika thandizo la mwamuna wakeyo, mayiyo amadya ndalamazo ndi mphongo zina osalabadiranso zoti ndalamazo ndi thukuta la munthu wina.  


Achibale komanso anthu ena omufunira zabwino mayiyo, anamudzudzula kuti asinthe khalidwe lakelo chifukwa tsiku lina adzalilira ku utsi, mwamuna wake akadzatulukira za zibwenzi zakezo.   

Pasanadutse nthawi atalandira malangizowo, mayiyo wapezeka ali ndi pathupi pomwe amuna onse omwe amayenda nawo akumusasa.  Mwamuna wake ku joni atamva nkhaniyi, wangolamula kuti asadzamupeze pakhomopo moti poopa kuyaluka wangosamuka mwakachete-chete  ku chithando-ko kupita kumudzi kwawo.  

Kumeneko anthu atamuona nkumva nkhani yake, akungomuseka kuti wachita zopusa malinga nkuti amayi ambili kumudziko amamusilira kuti mwamuna wakeyo amamutumizira ndalama zankhani- nkhani zomwenso amatha kuwatumizira makolo ake kumudzi. Pakadali pano mayiyo akukhalabe kumudzi kwawoko koma mosowa mtendere chifukwa nkhani yakeyo yawanda mdera lonselo, ndiye anthu akamuona akungomulozerana.

Get Your Newsletter