Bwalo la Magistrate ku Lilongwe likupitilira kumva mboni za boma pa mlandu wa a Norman Chisale, yemwe anali wachitetezo wa mtsogoleri opuma.
Nduna yoona za chilungamo, a Titus Mvalo, ndi imodzi mwa mboni yomwe yapereka umboni wake ku bwaloli.
Poyankhula pomwe amaperekera umboni wawo, a Mvalo anati mawu omwe oganiziridwa pa mlanduwu anayankhula pa wailesi ya kananema ya Zodiak akuti “Sindinaoneko chi minister cha bodza ngati ichi” komanso “onse ondizunza adzayankha” akuperekera chiopsezo komanso kunyazitsa ndunayi.
Iwo ati oganiziridwa pa mlanduwu anayankhula mawuwa chifukwa chakuti analembera ndunayi kalata yopempha kuti awalore kugwiritsa ntchito akaunti yawo yakubanki polipilira ana sukulu, zomwe a Mvalo akuti anali asanalandire kalatayi komanso sanali oyenerera kulowerera pa nkhaniyi.
Padakali pano, bwaloli layimitsa kaye mlanduwu ndipo likuyembekezekanso kudzamva kuchokera kwa mboni yomaliza ya boma.
Olemba: Madalitso Mhango