Khonsolo ya mnzinda wa Lilongwe yati siinamange malo okwelera bus aliwonse atsopano munzindawu ndipo malo aku Area 46 ku Grand Business Park ndi ongoyembekezera.
Mkulu wa Khonsoloyi, a Macloud Kadam’manja, ati bus zizigwiritsa ntchito kumadzulo amalowa osati malo akumvuma omwe anthu akugawana pamasamba amchezo, amene anati khonsoloyi idawakana.
Poyankhula ndi MBC Digital, a Aisha Sadala aku Blantyre, ati ntchito yodziwitsa anthu zamalowa siyinayende bwino.
Mayi Rashida Kadango aku Area 18 B munzinda wa Lilongwe ati malowa ndi abwino ngakhale ulendo wake ukulowa mnthumba.
“Ulendo omwe ndimalipira K1000 pano ndi K6000 kuti ndidzakwere bus, mwina tizolowera sikuti malowa ngoyipayi,” atero mayi Kadango.
Wapampando wagulu lowona zamaulendo apa bus la Public Transport Association a Moses Chauluka ati sakutsutsana ndi ganizo la khonsoloyi kuti nzindawu ukhalenso wamakono koma nthawi yowadziwitsa inachepa ndipo akuyembekezera kukumananso ndi akuluakulu aku khonsoloyi.
Khonsoloyi ikuyembekezeka kumanga malo akwerera bus amakono andalama zokwana k17 biliyoni.