Apolisi m’boma la Mchinji anjata m’busa wa Bua Abraham Africa yemwe dzina lake ndi James Solomon pomuganizira kuti anaba waya wa magetsi wa kampani ya ESCOM.
M’neneri wa apolisi Ku Mchinji, a Limbani Mpinganjira, ati a Solomon anawagwira m’bandakucha wa pa 12 March akusolola wayayu yemwe ndi wantali ndi ma mita 60, komanso ndi wa ndalama zokwana K297, 600 pa malo otchedwa Masautso m’bomali.
Malingana ndi a Mpinganjira, ati abusawa omwe ali ndi zaka 46 zakubadwa anagwirako ntchito ku ESCOM ndipo anapuma pa ntchito m’chaka cha 2019.
Owaganizirawa, amachokera m’mudzi mwa Chakuma kwa mfumu yaikulu Nkhumba m’boma la Phalombe ndipo akuyembekezeka kukaonekera kubwalo la milandu komwe akayankhe mlandu wakuba.
#MBCOnlineServices