Mamembala a magulu 16 a Community Savings and Investment Promotion (COMSIP) akonzetsa madesiki 65 pa sukulu ya pulaimale ya Chivutwe, imene ili m’mudzi wa Mdwala, kwa mfumu yayikulu Dzoole B m’boma la Dowa.
Anthuwa anakwanitsa kusonkha ndalama yokwana K800,000 kuti ntchitoyi ichitike pasukulupa, pomwe pali ophunzira 529 ndi madesiki 130 ndipo 87 mwa iwo ndi owonongeka, kutanthauza kuti ma desiki 43 ndi omwe anali bwinobwino.
Mphunzitsi wa mkulu wa pa sukuluyi, a Kenneth Mphanda, anayamika anthuwo kaamba kokonzetsa madesikiwo.
A Glamson Kachikonga, wapampando wa maguluwa, wati amene anakonza katundu wa sukuluyi adagwira ntchitoyi mwa ulele popeza ndi achinyamata amene anaphunzira ntchito ya ukalipentala ndi bungwe la COMSIP.
“Gulu lililonse linasonkha ndalama zokwana K50,000 zomwe pamodzi zinakwana k800,000 ndipo ndalama imeneyi tinagulira matabwa, misomali, zomatira ndi penti,” a Kachikonga anafotokoza.
Mkulu wa COMSIP Cooperative Union Limited, a Tenneson Gondwe, anati maguluwa agwiritsa ntchito upangiri wa bungwe lawo lomwe limasintha maganizo ma membala awo kuti apeze njira zothetsera mavuto omwe madera awo akukumana nawo.