Oyimba nyimbo za chamba cha Amapiano, Christopher ‘Avokado’ Malera wayamika Mulungu pomupulumutsa pa ngozi ya galimoto yomwe idachitika Lachiwiri m’mawa ku Mvera m’boma la Dowa.
Galimoto lake linawombana ndi wa njinga yamoto yemwe akuti amayenda mbali yake.
Koma Avokado wati sanavulale paliponse kupatulapo wanjingayo, amene wavulala mwendo ndipo akulandira thandizo pa chipatala chachikulu cha m’bomalo.
“Ubwino wake ndinamanga lamba wa galimoto langa lomwe linatembenuzika katatu,” iye anatero.
Katswiri oyimbayu posachedwapa adatulutsa nyimbo yotchedwa ‘Msandipitilire Yesu’.