Bwalo la milandu m’boma la Mangochi lalamula a Nelson Lipenga kuti akagwire ukaidi wa kalavula gaga kwa zaka makumi awiri (20) kaamba kopezeka olakwa pa mlandu ogwililira mwana wa zaka khumi ndi zisanu.
A Lipenga, amene ndi mphunzitsi, anzawo adawapezelera akuchita zadama ndi mwanayu pa nthawi imene anzake amawerenga.
M’bwalo la milandu, mtsikanayu adaulula kuti aphunzitsiwa akhala akugona naye mokakamiza kuyambira ali Standard 7 ndipo pano ali Standard 8 ndipo amaphunzira pa sukulu ya pulaimale ya Mama Khadidja, yomwe ndi ya atsikana okhaokha.
Ogamula mlandu, a Muhamad Chande, anati ndikutheka kuti a Lipenga adachita zimenezi ngati njira yobwezera chipongwe popeza mwana wawo adachitidwapo chipongwe choterechi.
Popereka chilango, a Chande adati limeneli likhale chenjezo kwa a bambo osaugwira mtima.