Davis Lungu wakhala wachinyamata wachinayi kupeza mpamba oyambila malonda wa ndalama zokwana K1 million yomwe ili muntchito yothandiza achinyamata 18 powapatsa K1 million aliyense kuti atukule ma bizinesi awo.
Ntchitoyi adakhazikitsa ndi wamalonda odziwika bwino, Triephornia Mpinganjira.
Lungu, yemwe ali ndi zaka 24 ndipo amakhala ku Zingwangwa mu mzinda wa Blantyre, ndipo wati ndalamayi agulira zipangizo zamakono zotsukira galimoto, mipando ndi kalapeti.
A Ephraim Nyondo amayankhula m’malo mwa a Mpinganjira, ndipo anati ndi okhutira ndi momwe ntchitoyi ikuyendera popereka mwayi kwa achinyamata omwe ali ndi malingaliro ogwira ntchito zamalonda koma akusowa poyambira.
Achinyamata ochita mphumiwa adasankhidwa pamene adapereka dongosolo la malonda awo kwa mayi Mpinganjira.