Apolisi m’dziko muno atsimikiza za imfa ya wapolisi mzawo Petros Mhango yemwe amagwira ntchito pa polisi ya Soche ku Blantyre.
Ofalitsankhani zapolisi m’dziko muno, a Peter Kalaya, wati a Mhango afa wapolisi mzawo atawaombera mwangozi pomwe amalimbana ndi mbava ku Chileka mu mzinda womwewo wa Blantyre.
A Kalaya ati apolisi anamvetsedwa kuti anthu ena akonza zokaba kunyumba kwa munthu wina ku Chileka ndipo anathamangira ku maloko komwe anayamba kuwomberana ndi mbavazo.
Mwatsoka, wapolisi wina anaombera a Mhango omwe anatsimikizika kuti afa atafika pachipatala chachikulu cha Queen Elizabeth Central Hospital.
Pakuwomberanako, apolisi awombera ndikupha mbava ziwiri pomwe zina zinathawa.