Boma lakhazikitsa magetsi oyendera mphamvu ya dzuwa ku nyumba ya malamulo pothana ndi vuto lakuthimathima kwa magetsi lomwe limasokoneza zokambilana za aphungu.
Nduna yoona zamphamvu zamagetsi, a Ibrahim Matola, yati kukhazikitsa magetsiwa, lomwe ndi gawo loyamba, zithandizira kuti nyumba ya malamulo isamaonongenso ndalama polipila ma bilo amagetsi a ESCOM.
Mwa zina, a Matola ayamika boma la India chifukwa chothandiza boma la Malawi pa ntchito zosiyanasiyana zachitukuko, kuphatikizapo mphamvu zamagetsi woyendera mphamvu ya dzuwa.
“Tiyamike Prezidenti wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera kamba koonetsetsa kuti vuto lakuthimathima kwa magetsi ikhale mbili ya makedzana mdziko muno. Magetsiwa ndi chitsimikizo kuti boma ndi lodzipeleka poonetsetsa kuti zokambilana za aphungu zikuyenda bwino. Anatelo a Matola.
M’mau ake, m’modzi mwa akuluakulu aku nyumba ya malamulo, a Funny Sibande, ayamika boma chifukwa chobweletsa mphamvu zamagetsi oyendera mphamvu ya dzuwa, ponena kuti mavuto omwe akhala akukumana nawo kamba ka vuto la magetsi ikhala mbili chabe.
Iwo ati aonetsetsa kuti katunduyu akutetezedwa.
M’modzi mwa akuluakulu a kampani ya International solar Alliance (ISA) yaku India yomwe yagwira ntchito ndi thandizo la ndalama zokwana $50,000 a Jaspal Sigh ati apitiriza kugwira ntchito yokhazikitsa magetsiwa m’dziko muno ngati mbali imodzi yolimbikitsira ubale pakati pa maiko a Malawi ndi India.
Magetsi amphamvu ya dzuwa, omwe ndi pafupifupi 25 kilowatts, adzigwila ntchito masana kunyumba ya malamulo pamene a ESCOM adzigwila ntchito madzulo okha.