Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Unduna uchenjeza ochita malonda mwachinyengo

Unduna wa Zamalonda ndi Mafakitale wachenjeza ochita malonda onse amene akugulitsa shuga pa mitengo yokwera kwambiri komanso yosavomerezeka kuti adzatsekeredwa mashopu awo ndipo adzayankha milandu pophwanya malamulo a dziko lino pa malonda.

Izi zadza pamene chipikisheni chomwe undunawu, mogwirizana ndi bungwe loona kuti pasamakhale kuponderezana pa ntchito za malonda pa msika la CFTC, watseka ma shopu ena m’boma la Lilongwe kaamba kogulitsa shuga pamitengo yokwera kwambiri komanso yosavomerezeka.

Undunawu wati mtengo ovomerezeka wa belo la shuga la mapaketi 20 ndi K37,500 pamene paketi imodzi ya shuga mtengo wovomerezeka ndi K2250.

Ena mwa ma shopu omwe atsekedwa ndi Romana Trading komanso Chou Chou ku Area 2 (Bwalo Lanjovu), Shalom Shop Ku Area 25 (Nsungwi) komanso Simama General Dealers ku Area 25 (Nsungwi).

Mchikalata chomwe asayinira Mlembi mu Unduna wa Zamalonda ndi Mafakitale, Christina Zakeyo, boma lati sililola kuti anthu m’dziko muno adziberedwa pogulitsidwa shuga pamitengo yosavomerezeka.

Chikalatachi chapempha anthu m’dziko muno kuti azidziwitsa undunawu za amalonda onse omwe akuchita mchitidwewu.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Tsopano ndikupeza bwino-Ras Kansengwa

Lucius anali katswiri, watero ‘Reggae Ambassador’ Charles Sinetre

Simeon Boyce

A Nankhumwa akhazikitsa chipani

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.