Pofuna kuwonetsetsa kuti achinyamata amene amaliza maphunziro a ulimi wa zipatso, masamba, maluwa ndi mbewu zina pa sukulu ya Corporate Institute of Horticulture (CIH) ali ndi mpamba oyambira malonda, bungwe la Technical Entrepreneurial and Vocational Education and Training Authority (TEVETA) lagwirizana ndi banki ya FDH kudzanso bungwe la National Economic Empowerment Fund (NEEF) kuti lithandize anyamata omwe amaliza maphunziro ndi ngongole.
Mkulu wa bungwe la TEVETA m’chigawo cha pakati, a Joseph Sambaya, anena izi m’boma la Salima pomwe amapereka ma satifiketi kwa achinyamata omwe amaliza maphunziro a ulimi wa zipatso pa sukuluyo.
Peter Mlangali, mmodzi mwa ophunzira omwe amaliza maphunziro, wati ngongoleyi ithandiza achinyamatawa kupeza nawo mwayi wochita malonda pa misika ya m’dziko muno ndi misika yakunja kamba koti akhala ndi mpamba okwanira.
Wolemba Aisha Amidu