Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Tithetse katangale kumasewero – ACB

Bungwe lothana ndi ziphuphu ndi katangale m’dziko muno la ACB lati kumpira kumachitika zachinyengo zosiyanasiyana zimene zikupangitsa kuti zamasewero zisamapite patsogolo.

Mkulu wa bungweli, Martha Chizuma, wanena izi ku Lilongwe pomwe amasayinira pangano la mgwirizano pakati pa bungwe la ACB ndi bungwe loyendetsa mpira wamanja m’dziko muno la Netball Association of Malawi(NAM).

Malinga ndi a Chizuma, mgwirizanowu uthandiza kwambiri kuti masewero a mpira wamanja apite patsogolo ati kaamba koti nthawi zambiri kukapezeka ndalama, anthu oyendetsa mabungwewa amatha kulowetsa chinyengo, zomwe zimachotsa mtima olimbikira mwa osewera.

Iwo atinso kafukufuku yemwe adapanga akuonetsa kuti nthawi zina kaamba ka chinyengo, osewera ena aluso amatha kusapatsidwa mpata ndi aphunzitsi ndipo ati ena amatha kukakamizidwa kuchita mchitidwe ogonana ndi aphunzitsi kuti adzikonderedwa, zomwe akuti kudzera mumgwirizanowu achita chothekera kuzithetsa.

M’mawu ake, wapampando wa bungwe la NAM, a Abigail Sheriff, wati ndiokondwa kuti bungwe la ACB labwerapo kuti lithandizane ndi bungweli pothetsa mchitidwe wachinyengo.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

FIRST CAPITAL BANK LAUNCHES 5 MITA IPITE PROMOTION

McDonald Chiwayula

STIs on the rise globally – WHO

MBC Online

Committee announces closure Tobacco selling season

Earlene Chimoyo
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.