Mwini wake wa kampani ya New Dawn Boxing promotion, Michael Chimaliza, wapempha mabungwe komanso kampani zosiyanasiyana m’dziko muno kuyika chidwi potukula masewero omwe amaoneka ngati ang’onoang’ono, ponena kuti pali achinyamata ochuluka amene anapanga chisankho chosamala miyoyo yawo kudzera kumasewerowo.
Chimaliza wanena izi pomwe amalandira thandizo la ndalama zokwana K6 million yomwe kampani ya SICO Holdings yapereka ku New Dawn Boxing promotion kuti ithandizire zokonzekera za nkhonya yomwe ichitike pa 2 June mumzinda wa Lilongwe.
A Chimaliza ayamikira kampaniyo kaamba koti imayika chidwi pothandiza nkhani zamasewero, makamaka nkhonya.
Ndipo mkulu wa SICO Holdings, Mathews Mughogho, ati ndiodzipereka kuthandiza ochita masewero achisodzera ndipo wapempha achinyamata kuti adzisunga mwambo kuti luso lawo lidzipita patsogolo.