Bungwe la ESCOM lati makina ake a magetsi anadzithimitsa lero nthawi itatsala mphindi 18 kuti ikwane 12 koloko masana.
Malinga ndi chikalata chomwe a ESCOM atulutsa, pakadali pano iwo akuyesetsa kubwezeretsa magetsi m’madera ambiri ngakhale m’madera ena magetsi sanayakebe.
Iwo ati pomwe akufufuza kuti apeze chomwe chinachititsa kuti magetsi azime, akuyesetsanso kubwezeretsa komwe sanayambe kuyaka.