Dziko la Malawi lati liri ndi chiyembekezo choti likwaniritsa ntchito zamgwirizano ndi maiko onse a m’bungwe la SADC.
A Adwell Zembere omwe akutsogolera nthumwi za dziko la Malawi pa msonkhano ounika momwe mabungwe omwe siaboma angagwilire ntchito zawo poonetsetsa kuti maiko a m’bungweli akukwaniritsa zopititsa patsogolo ntchito zosiyanasiyana kuphatikizapo zaumoyo, zaulimi komanso zachitukuko anena izi mu mzinda wa Harare mdziko la Zimbabwe.
A Zembere ati ngakhale kuti dziko la Malawi lakhala likukumana ndi zovuta zosiyanasiyana monga ng’amba ndi anamondwe koma likuyesetsa kuti lichite bwino.
“Tiyenera kukhazikitsa ndondomeko yoyenera yomwe ingathandize kuti pakhale njira zoperekera malipoti a momwe zinthu zikuyendera,” anatero a Zembere, posonyeza kufunikira kwa kalondolondo ndi kupereka malipoti pamene dziko likupita patsogolo ndi mfundo zamgwirizano wa maiko a mu SADC.
Mmodzi mwa amkhalakale pantchito ya utolankhani komanso membala wa bungwe la African Union Agenda 2063 Media Network, a Sydney Katunga Phiri, anavomezera kufunikira kwa mgwirizano pakati pa akuluakulu aboma, mabungwe omwe siaboma ndi atolankhani kuti mfundo zomwe zakwanilitsidwa zifalitsidwe mwadongosolo.
“Ntchito yofalitsa uthenga ndiyofunika kwambiri maaka pamene maiko akuchita migwirizano yosiyanasiyana. Uthenga umayenera kukonzedwa bwino kuti ukhale womveka bwino Kwa anthu. Pakadali pano bungwe la African Union Agenda 2063 Media Network likuyenera kutenga nawo mbali pa ntchitoyi monga dongosolo laulimi la Comprehensive Africa Agriculture Development Programme (CAADP) ndi ndondomeko zina za maiko a mu Africa zikuyenera kufikira anthu ambiri,” anatero a Phiri.
Nthumwi za dziko la Malawi pa msonkhanowu ndikuphatikizapo akuluakulu a unduna wa zachuma, unduna woona zaubale ndi maiko ena, ndi mabungwe omwe siaboma monga bungwe la National Smallholder Farmers’ Association of Malawi (NASFAM), Malawi Economic Justice Network (MEJN), Malawi. Health Equity Network (MHEN), Edukans komanso Council for Non-governmental Organisations.
Nthumwizi zitakambirana m’magulu amaiko omwe zachokera, zikupereka malipoti komanso dongosolo la momwe akwaniritsire ntchitozi mpaka msonkhano wotsatira.
#MBCDigital #Manthu