Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Tikupha makwacha – TAMA

Bungwe la alimi a fodya la Tobacco Association of Malawi (TAMA) Trust lati alimi a fodya ndiwokondwa chaka chino kamba koti akupha makwacha ndi mitengo yabwino yafodya yomwe ogula akupereka.

Mtsogoleri wa TAMA, a Abel Kalima Banda, awuza MBC Digital kuti chiyambireni msikawu chaka chino, mitengo yakhala ikukwera.

Iwo alonjeza kuti alimi apitiriza kupititsa fodya wabwino ku msikawu.

Pakutha sabata zisanu ndi ziwiri, alimi mdziko muno apeza ndalama zokwana K327 billion kuchokera ku fodya.

Related posts

Gulu la alimi lapeza K620 million kudzera mu ulimi wa nzimbe

Rabson Kondowe

TIGWIRANE MANJA NDI BOMA PA CHITUKUKO -MATOLA

MBC Online

Tambala Super Cup ayikhazikitsa

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.