Malawi Broadcasting Corporation
Development Health Local Local News Nkhani

Tifalitse uthenga wa matenda a TB ndi Khate — Madam Chakwera

Mayi wa pfuko lino, Madam Monica Chakwera, apempha mzika za dziko lino kuti zitenge gawo pofalitsa uthenga okhudza chifuwa chachikulu (TB) komanso khate.

Iwo anamema a Malawi ku nyumba ya chifumu mu mzinda wa Lilongwe pamene, mogwirizana ndi Paradiso TB Patients trust, amakumana ndi anthu pafupi-fupi 100 amene anadwalako ndi kuchira matendawa.

Madam Chakwera anati kuti izi zichitike, pakufunika m’gwirizano pa nkhondo yolimbana ndi matendawa kuphatikizapo kufalitsa uthenga okhudza izi ndipo iwo anati ndi okondwera poona kuti chiwerengero cha anthu odwala TB komanso Khate chikuchepa.

Dr James Mpunga, amene ndi mkulu oona za matendawa m’dziko muno, anayamikira boma poonetsetsa kuti mankhwala a chifuwa cha chikuluchi alipo m’dziko muno.

Izi zili chomwechi pamene kwa zaka khumi tsopano, malinga ndi Dr Mpunga, dziko lino lakhala ndi mankhwala okwanira komanso a pamwamba zedi, zomwe zili molingana ndi m’mene zinthu zikusinthira.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

SPEAKER SUSPENDS HOUSE BRIEFLY

MBC Online

GOVT LAUDS MARANATHA ACADEMY

McDonald Chiwayula

Fumbi koboo kumwambo wa Prison Health Day

Yamikani Simutowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.