Malawi Broadcasting Corporation
Entertainment Local News Nkhani

“Tidzikondana tili moyo”

“Ndikofunika kuti a Malawi adzikondana komanso kuthandizana pa mavuto ndi mtendere,” awa ndi mawu amene anena ndi eni ake a kampani ya Sosten Motors, a Sosten Kapeni.

Iwo amayankhula izi pamene amachingamira katswiri ojambula zithunzi m’dziko muno, Ras Peter Kansengwa, pa bwalo la ndege la Kamuzu mu mzinda wa Lilongwe.

Kansengwa adali m’dziko la India kumene amalandira thandizo pa chipatala cha Artemis.

A Kapeni apereka ndalama yokwana K500,000 kwa a Kansegwa kuti adzigwiritsa ntchito pa moyo wawo.

“Zimakhala zokhudza kuona anthu akuthandiza kwambiri pamwambo wa maliro, chonsecho munthu wakhala akuvutika ali moyo,” iwo anatero.

Ras Kansengwa anayamikira boma komanso aMalawi amene akhala akuwathandiza pamene adali m’chipatala kulandira thandizo kwa mwezi ndi theka.

M’mbuyomu, iwo adalinso m’dziko la India kumene adakalandira opaleshoni ya diso.

 

Related posts

Mafumu ku Mzimba apepesa Dr Chakwera

Romeo Umali

Boma lati alimi atha kukolora zochuluka

Romeo Umali

FDH Bank Cup Preliminary Draw set for today

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.