Katswiri watsopano womwetsa zigoli wa timu ya Mighty Mukuru Wanderers yemwe kwawo ndi ku Cameroon, Sama Thierry Tajong, ndi wokayikitsa ngati asewere nawo Blantyre Derby kaamba koti sanalandilmrebe chilolezo chosewera mpira kapena kugwira ntchito mdziko muno (Work permit) pa chingerezi.
Kumayambiliro kwa sabata ino, Tanjong anasaina mgwirizano wa zaka ziwiri ndi timu ya Wanderers.
Padakali pano timu-yi ikuyesetsa kuti katswiri-yu apeze chilolezo chosewera masewero ake woyamba pomwe Wanderers ikukumana ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets masanawa mu ligi ya TNM.
Olemba Amin Mussa