Malawi Broadcasting Corporation
News Nkhani

SHUGA ADZIPEZEKA OKWANIRA – ILLOVO

Kampani yopanga ndikugulitsa shuga ya Illovo yati anthu asade nkhawa ndikusowa kwa shuga komwe kwakhalapo pakatipa,ponena kuti vutoli litha.

Akuluakulu a kamaniyi anena izi mu mzinda wa Blantyre pamene Illovo ikufotokoza za m’mene ntchito zake zayendera m’miyezi isanu ndi umodzi, kuchoka mu September chaka chatha mpaka February chaka chino.

Mkulu wa Illovo a Lekani Katandula ati vuto lakusowa kwa shuga labwera kamba ka mavuto osiyanasiyana, kuphatikizapo kuti kampaniyi inapanga shuga ochepa.

A Katandula ati mwazifukwa zina, Illovo inapanga shuga ochepa kamba koti minda ya nzimbe inawonongeka ndi namondwe.

Iwo anawonjezera kuti shuga anasowanso kamba koti ochita malonda amatenga shuga wambiri kukagulitsa ku mayiko oyandikana ndi dziko lino, kamba koti shuga waku Malawi ndiwotsika mtengo poyerekeza ndi mayikowa.

Komabe iwo ati a Malawi asadandaule kamba koti achilimika pofuna kuthetsa mavutowa ndipo ayamba kupanga shuga ochuluka kuti mdziko muno mukhale shuga okwanira.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Pezani nkhani za MBC pa WhatsApp kapena SMS

MBC Online

UDF COMMENDS CHAKWERA’S ADMINISTRATION ON PRIORITIES

MBC Online

Kuli ufulu wa demokalase ku MCP— Chilondola

Mayeso Chikhadzula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.