Komiti yagulu la nthambi zosiyanasiyana yoona za mbewu zazikhawo monga Chinangwa ndi Mbatata yati pakufunika kusintha maganizo pankhani ya chakudya chomwe dziko lino limadalira.
Wapampando wa komitiyi, a Jean Pankuku, wayankhula izi ku Lilongwe pomwe komitiyi imakumana ndi alimi komanso akuluakulu aku unduna wazaulimi.
“Tikufunika kuyika chidwi ku ulimi wa mbewu zotere chifukwa nyengo siikupanganika. Boma liganizire zoyika ndondomeko zazipangizo zotsika mtengo ku ulimi wazikhawo osati chimanga chokha,” atero a Pankuku.
M’modzi mwa akuluakulu ku unduna wa zaulimi, a Alfred Mwenefumbo, wati ndi zomvetsa chisoni kuti ambiri amatenga ulimiwu ngati chongophelera chabe pomwe mvula yachita njomba.
A Mwenefumbo apempha alimi kuti abwere pamodzi ndikuyamba kuchita ulimiwu pa mlingo waukulu ndikumapha makwacha kaamba koti misika ilipo kale yopezekeratu.