A Eisenhower Mkaka omwe ndi mlembi wamkulu wa chipani cha MCP ayamikila m’tsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera kaamba kopititsa patsogolo ndale za demokalase.
A Mkaka ati Dr Chakwera amasankha anthu m’maudindo potengela nzeru zao osati ndale ndipo ati izi zili chomwechi kutsatira pamene anthu ambiri ochoka m’zipani zina akulowa chipani cha Kongolesi chifukwa iwo akuchita zakupsya posintha dziko lino pa chitukuko.
Iwo ayamikanso ntchito yaikulu yomwe alimi akugwira m’dziko muno pothandizila kuti m’dziko muno mudzipezeka ndalama za kunja.