Oyimba nyimbo za uzimu ati ndi okondwa ndi momwe nzika za mu nzinda wa Lilongwe zinabwelera pa phwando la maimbidwe limene linachitikira ku Sheaffer lolemba pa 8 July.
Mwambowu anaukonza pofuna kupeza thandizo la ndalama zothandizira oyimba nzawo, Peter Mlangeni, amene akufunikira ndalama zokwana K15 million kuti apeze thandizo lachipatala loyenera.
M’modzi mwa otsogolera gulu la oyimbawa, a Norman Phiri, ati akudziwa kuti ndalama yomwe akufuna sangaipeze pakamodzi koma ati ali ndi chikhulupiliro kuti zitheka ndithu.
Pa phwando la maimbidweli, anthu ambiri omwe analiko anaonetsa kukhutira kwawo ndi maimbidwe a akatswiri osiyanasiyana kuphatikizapo McDonald Mlaka Maliro, Shammah Vocals, Great Angels Choir, Chippo Nyirongo, Milefa Sisters, Evance Meleka ndi Lulu kungotchulapo ochepa.
Oyimbawa, ati pofuna kupereka mpata kwa anthu a ku Blantyre, akhalanso ndi mwambo ngati omwewu pa 28 July.