Wachiwiri kwa Chancellor wa sukulu ya ukachenjede ya Malawi University of Science and Technology (MUST), Professor Address Malata, wati atsikana onse omwe anawasankhira ku sukuluyi ndipo analephera kuyamba maphunziro chifukwa cha kusowa kwa ndalama zolipilira sukulu apite akayambe chifukwa ndalama zapezeka.
Professor Malata auza MBC kuti zoti atsikana adzisiya sukulu chifukwa chosowa malipiro MUST siikupanga nawo.
Iwo anena izi pamene kampani ya Illovo Sugar Malawi imaperaka ndalama zokwana K250 million ku thumba lothandizira ophunzira osowa, makamaka atsikana.
Iwo ati padakali pano, kuthumbali kuli ndalama zokwana K400 million.