Mtsikana wa zaka 17 yemwe wapambana mphotho ya mtsikana yemwe akuoneka nditsogolo lowala mu COSAFA, Leticia Chinyamula, walangiza anzake omwe amachita masewero osiyanasiyana m’dziko muno kuti asamangodalira mpira okha koma adzithanso kuphunzira zinthu zina zomwe zingawathandize atakumana ndi mavuto pantchito yawo.
Chinyamula wanena izi atangofika kumene kuchokera m’dziko la South Africa komwe walandirako mphothoyi atagonjetsa anzake awiri omwe amapikisana nawo, Rose Kadzere wa timu ya Scorchers komanso Esther Banda wadziko la Zambia.
“Ndine okondwa kupambana mphothoyi ndipo ndikhumbo langa kuti ilimbikitse atsikana onse kuti ndizotheka. Pempho langa kwa osewera anzanga ndiloti tidziyesetsa kulimbikira, makamakanso kukhala ndi chidwi pamaphunziro poti mpira ndintchito yakanthawi kochepa,” iye anatero.
Naye Rose Kadzere, yemwe ku Malawi kuno amaseweranso limodzi ndi Leticia kutimu ya Ascent academy, wati ndiokondwa kaamba koti mwa osewera ochuluka omwe ali pansi pa COSAFA, iye anasankhidwa kupisana nawo.