A polisi amanga munthu mmodzi ogwira ntchito ku bungwe la ADMARC ndi ena awiri powaganizila kuti anazembetsa matumba a chimanga okwana 300 m’boma la Machinga.
Ofalitsa nkhani za apolisi mchigawo chakumvuma, a Patrick Mussa, ati amanga a Malani Kaira a zaka 35 a ku bungweli, komanso a Isaac Bisayi a zaka 39 komanso a Imran Mtambo a zaka 30.
A Mussa ati a Bisayi omwe ndi dalaivala wa galimoto yaikulu, anapachila matumba achimanga okwana 600 kuchokera pa ADMARC ya Dowa, omwe amayenela kukawatsitsa ku Nkwepele m’bomali, koma mmalo mwake anakatsitsa matumba 300 pakhomo pa Imran Ntonda ku Ntaja.
Iwo ati atatuwa, awatsegulira mulandu ogwirizana pofuna kuba komanso wina okuba.
#mbconlineservices