Eunice Katunga wa ku Lunzu m’dela la Group Village Headman Kumponda mfumu yaikulu Kapeni m’boma la Blantyre wati moyo wa banja lake wasintha potsatira ntchito yootchelera zitsulo ‘Welding’ pachingerezi yomwe akugwira ku dela la kwawo.
Eunice ndi mmodzi mwa achinyamata okwana 721 ochokera m’maanja omwe amalandira mtukula pakhomo komanso nthandizi wa mbwezera chilengedwe ndipo ali m’magulu osunga ndi kuchulukitsa ndalama a COMSIP omwe anaphunzitsidwa ntchito za manja zosiyanasiyana mu gawo loyamba la ntchitoyi ndipo anapatsidwa zida zogwilira ntchito yawo.
Iye analandiranso ngongole ya ndalama zokwana K500,000 kuchokera ku COMSIV yomwe ndi nthambi yoona za chuma ku COMSIP zomwe anagulira zipangizo zogwilira ntchito yake.
“Chiyambireni kupanga bizinesi yanga mokhazikika mwezi wa April, ndikumakwanitsa kupeza ndalama tsiku ndi tsiku chifukwa anthu amabwera kudzafuna kuotcheleletsa njinga, kupangitsa makasu, nkhwangwa, komanso mafelemu a zitseko ndi mawindo. Chakudya ndi zofunika zina pakhomo panga sizikusowa ndipo ndikutha kusamalira banja langa mosavuta,“ watero Eunice.
Eunice wakwanitsanso kupezetsa mwayi wa ntchito wachinyamata nzake yemwe akuthandizana naye kuotchelera zinthu zosiyanasiyana.
Malinga ndi a Judith Msusa, mkulu woyang’anira achinyamata mu unduna wa za achinyamata ndi masewero, boma ndi lokondwa kuti bungwe la COMSIP lapereka luso komanso mpamba kwa achinyamata omwe anali ovutikitsitsa omwe amadalira ntchito za nthandizi pa umoyo wao ndipo pakadali pano apeza ntchito zodalirika.
Ndipo mkulu woyendetsa ntchito za bungweli, a Suzen Kondowe, wati achinyamata omwe anaphunzira ntchito za manjawa akhazikitsa magulu – ma cooperative — okwana 32 omwe adzipanga zinthu za luso zogwirizana ndi zomwe akufuna.
Achinyamata okwana 1, 627 akuyembekezeka kuyamba maphunziro onga awa mu gawo lachiwiri la ntchitoyi pofika mwezi wa June chaka chino kuchokera mmaboma 14 komwe ntchitoyi yafikira owe ndi kuphatikizapo Chiradzulu, Blantyre, Dowa, Kasungu, Rumphi ndi Chitipa.