Apolisi ku Mangochi ati chiwerengero cha ngozi zapamsewu zikuchuluka m’bomali.
Ofalitsankhani za Polisi ya Mangochi, Amina Tepani Daudi, wati kuchokera mwezi wa January 2024 kufika pano ali ndi chiwerengero cha ngozi 41, zomwe 25 mwa izo zikukhudza njinga zamoto.
Pa ngozi zimenezi, ana 13 anafa mwa anthu onse 29 omwe adafa.
Daudi wayankhula izi pamene apolisi m’bomali apempha amipingo yosiyanasiyana monga Mpondasi Seventh-Day, Katolika, CCAP komanso Baptist, omwe azungulira tauni ya Mangochi, kuti athandize kufalitsa uthenga wakayendedwe kabwino kapamsewu.
“Boma la Mangochi lili ndi chiwerengero chochuluka cha anthu omwe amayenda panjinga zamoto komanso zakapalasa kotero tikukhulupilira kuti mipingo ili ndi udindo otithandiza kufalitsa mayendedwe abwino apamsewu kuti ngozi zichepe,” anatero Daudi.
Apolisiwa awuza MBC kuti apitiriza kugwira ntchito yophunzitsa anthu mayendedwe abwino apamsewu.