Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Sports Sports

Ndidzakutumizani Ku Mangalande – Apostle Kawinga alonjeza timu ya CRECK

Mtsogoleri wa timu ya CRECK Sporting, Apostle Clifford Kawinga, walonjeza kupitiriza kusamalira osewera ndi aphunzitsi a timuyi ngati angapitirize kulimbikira ndikuchita bwino mu ligi yaikulu ya TNM.

A Kawinga amayankhula pomwe anakonzera timuyi mgonero madzulo alachinayi ngati njira imodzi yowayamikira ndikuwalimbikitsa pa momwe ayambira mu ligiyi.

A Kawinga ati ali ndi loto lopititsa timuyi ku maiko akuulaya monga ku Mangalande kukapuma komanso kukasewera masewero opimana mphamvu ndi matimu ena.

Iwo ati ali ndi anthu omwe amalumikizana nawo m’maikowa ndipo nkosavuta kuti izi zitheke.

Pomwe malikhweru ndi majowajowa analimkati kamba ka nkhaniyi, osewerawa anakuwanso mfuwu wachimwemwe pomwe mtsogoleri wawoyu analengeza ndikuyamba kupereka K100,000 kwa osewera ndi aphunzitsi onse ndikulonjeza kuti zokoma zambiri zikubwera, kuphatikizapo kuika osewerawa pa ndondomeko ya za umoyo (medical scheme).

Mphuzitsi wa timuyi, McDonald Mtetemera, wati anyamatawa awatemera mangolomera ndipo achita chilichonse chothekera kuti timuyi ichite zakupsa mu ligi yaikuluyi.

CRECK inagonjetsa matimu a Mighty Tigers komanso Moyale Barracks m’masewero ake awiri oyamba isanagonje ndi Might Mukuru Wanderers ndipo kumathero asabata ino ikumana ndi Mzuzu City Hammers.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

CENTRE FOR AGRICULTURAL TRANSFORMATION BAGS INTERNATIONAL AWARD

MBC Online

Bushiri Foundation seals deal with Nigerian actor Nkem Owoh

Eunice Ndhlovu

93 Ethiopians, Malawian Arrested for Contravening Immigration Laws

Alick Sambo
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.