Bungwe lotchedwa We Effect, lomwe limagwira ntchito ndi alimi ang’ono ang’ono omwe ali m’magulu, lalimbikitsa alimiwa kuchita malonda ena apadera posadalira ulimi okha pofuna kupeza phindu lochuluka komanso kukhala ndi chakudya chokwanira.
Mkulu wa bungwe li m’dziko muno, a Easter Chirwa, anena izi kwa Kalonga m’boma la Salima pomwe adayendera ntchito zomwe bungwe lawo likugwira.
Izi zikudza pamene alimi ochuluka akhudzidwa ndi mavuto odza kamba ka kukusintha kwa nyengo.
Wapampando wa gulu la amayi osoka zovala la Tikondane, a Grace Liwonde, omwe adalandira thandizo la makina osokera kuchokera ku bungwe li, ati moyo wawo wa tsiku ndi tsiku wasintha kuchokera mu phindu lomwe amalipeza akagulitsa zovala zomwe iwo amasoka.
A Liwonde anafotokozanso kuti akuyembekeza kupha makwacha akakolora mbewu zawo, zomwe akutinso ziwonjezera mpamba wa malonda awo pokuza misika yomwe ali nayo pakadali pano.
Amayi wa akupindula ndi bungwe la We Effect kudzera mu ntchito yawo yotukula amayi ndi achinyamata omwe amalima thonje ya Women Economic Empowerment for Cotton Value Chain.