Akatswiri pa nkhani za malonda a zachuma ati akukhulupilira kuti kutsegulira kwa msika wa fodya mwezi wamawa kutha kuthandizira kuti ndalama yakwacha ikhazikike.
Iwo anena izi pamene banki yayikulu ya Reserve yalengeza kuti mtengo ogulira ndalama ya dollar tsopano wafika pa K1,751 malinga ndi msika wa ndalamayi, umene unachitika lolemba sabata ino.
Mtsogoleri wa bungwe la akatswiriwa, a Leslie Fatch, ati kutsika kwa mphamvu ya ndalama ya kwacha chaka chatha komanso kwapanoku kutha kupangitsa kuti katundu monga fodya akhale ndi mtengo wabwino muma dollars, zomwe zitha kupangitsa kuti kwacha ikhazikike kamba koti ndalama zakunja zikhalamo zambiri m’dziko muno.
Koma a Fatch ati izi ziwoneka bwino fodyayu akayamba kufika pa msika kamba koti nyengo ya El Nino itha kupangitsa kuti alimi akolore fodya ochepa.
Katswiri wina, a Bond Mtembezeka, ati vuto ndilakuti dziko lino likuyitanitsabe katundu wambiri kuchokera kunja yemwe amafunika ndalama zambiri zakunja, pamene kapezedwe kake ka ndalama zakunja sikanasinthe kweni kweni.
Komabe iwo ati pamene alimi ayambe kukolora komanso msika wa fodya kutsegulidwa, zinthu zitha kusintha.