Alimi a fodya ayamikira boma komanso bungwe lotolera misonkho la Malawi Revenue Authority (MRA) powabwezera ndalama zokwana K9. 4 billion zamsonkho omwe akhala akudulidwa akagulitsa fodya ku msika wovomerezeka wa fodya.
Izi zadziwika pamsonkhano wa alimiwa mumzinda wa Lilongwe.
Oimira alimiwa, GVH Kasangazi ati zomwe lachita bungwe la MRA zawonetsera poyera kuti boma likufuna kuti alimi adzipindula pantchito yawo, ponena kuti alimiwa samadziwa msonkho woyenera kuti adulidwe.
Wachiwiri kwa komishonala wa bungwe la MRA, a Janet Kholowa, ati boma laika ndondomeko yatsopano yoti alimiwa asamavutike ndikubwera kumaofesi a bungweli kuti abwezeredwe ndalama.
“Mukhoza kuona kuti pa makalabu 14,800 ndiye kuti ndi alimi osachepera 148,000 omwe timayenera tiunike ngati anapeza phindu kapena ayi tisanawabwezere ndalama. Koma tsopano kuyambira mchaka cha 2021 tikungodula 1 percent ndipo tikatero tathana,” anatero a Kholowa.
Ndalama yokwana K14.9 billion ikubwezeredwa kwa alimi ochokera m’makalabu 14800 m’dziko muno, omwe akhala akudulidwa msonkho kuyambira m’chaka cha 2014 mpaka 2020.