Apolisi ku Namwera m’boma la Mangochi atsekera m’chitokosi a Nelson Lipenga azaka 49 zakubadwa powaganizira kuti akhala akugwilira ophunzira wa zaka 15 wa Standard 8 pasukulu ya pulaimale ya Mama Khadija, yomwe ndi ya atsikana okhaokha.
Ofalitsa Nkhani za Polisi ya Mangochi, a Amina Tepani Daudi, watsimikiza nkhaniyi ndipo wati oyang’anira atsikanawa ndiye adawapezelera anthuwa nthawi yamadzulo atatsekerana m’chipinda china ndipo panthawiyi mtsikanayu amayenera kukhala m’chipinda chowerengela limodzi ndi amzake.
Nkhaniyi itapita ku Polisi, mtsikanayu anaulula kuti anthuwa adayamba kugonana chaka chatha iyeyu ali Standard 7.
A Lipenga awatsegulira mulandu ochita zadama ndi mwana ndipo akaonekera ku khoti apolisi akatsiriza kufufuza za nkhaniyi.