Ndalama ya Kwacha yakhazikikabe pa mtengo wa K1751 pogula ndalama ya Dollar imodzi pomwe inafika mu March chaka chino.
Izi ndi malinga ndi msika wa ndalama zakunja omwe banki ya Reserve inachititsa lachinayi sabata yatha omwe banki zisanu zinachita nawo.
Ndalamayi ikuyembekezeka kupitilira kukhazikika pamene ndalama zakunja zochokera ku fodya pano zakwana $182 million (pafupifupi K318 billion).