Prophet Shepherd Bushiri wagawa chimanga kwa Nchilamwera m’boma la Thyolo komwe wapempha anthu kuti asalowetse ndale pa thandizo lake.
Mneneri Bushiri wati apitirizabe kupereka chimanga kwa anthu okhudzika ndi njala m’madera onse m’dziko muno, pomwe mabanja oposa 40,000 tsopano alandira chimangacho.
Mneneriyu wapemphanso amfumu a Nchilamwera kuti adziwitse a khonsolo ya bomali kuti ngati angamulole, athandize pantchito yomanga technical college pa boma la Thyolo.