Mafumu ayamikira mtsogoleri wa dziko Dr Lazarus Chakwera pantchito za chitukuko zomwe akuchita mzigawo zonse za dziko lino.
Poyankhulapo m’boma la Dowa, Senior Chief Chiwere, yati kudzera mu utsogoleri wa Dr Chakwera, dziko lino likhala ndi chitukuko chapamwamba. Izi ati ndi zomwe zikusintha miyoyo ya anthu ambiri.
Iwo athokozanso mtsogoleri wa dziko lino pokhala odzichepetsa ndi kumacheza ndi anthuwa.
Mfumuyi yapempha mtsogoleri wa dziko lino kuti ntchito ya madzi akumwa ya Salima-Lilongwe Water Project itheke popeza ati anthu a mderali amavutika kuti apeze madzi abwino akumwa.
Iwo apemphanso boma kuti liwathandize kuti chimanga chidzipezeka mosavuta m’misika ya ADMARC.
Wolemba: Beatrice Mwape ndi McDonald Chiwayula.
#mbcmw