Mkulu wamajaji m’dziko muno, a Rizine Mzikamanda, ati komiti yatsopano yoona milandu ya chisankho yomwe anayikhazikitsa idzithandiza kuyendetsa mwamsanga komanso mwachilungamo milandu yamtunduwu ikachitika.
A Mzikamanda ati anatenga nzeru zokhazikitsa komitiyi kuchokera m’dziko la Kenya lomwenso lili ndi anamandwa pankhani yoyendetsa chisankho motsata malamulo.
“Titapita chaka chatha ku Kenya mwezi wa December tidasilira ndi momwe anzathuwo amayendetsera nkhani zokhudza kusamvana pachisankho kotero nafe January chaka chino takhazikitsa [komiti] yathu,” anatero a Mzikamanda.
Bungwe loyendetsa chisankho mdziko muno la MEC ndi thandizo lochoka ku UNDP linakonza mkumano ndi majaji aku Malawi ndi Kenya kuti agawane nzeru posanthulanso zisankho za 2019 ndi 2020.
Mmawu ake, wapampando wa MEC, Justice Chifundo Kachale, wati ali ndichikhulupiliro kuti mkumanowu ubala zipatso ndikuthandizanso kubwezeretsa chikhulupiliro pakati pa anthu ovota, maka pakayendetsedwe kachisankho.
“Anthu ovota safuna kudikira nthawi yayitali maka pamilandu yachisankho kotero komitiyi ithandiza kuwunikira zinthu ngati zimenezi pomwe tikulunjika 2025,” atero a Kachale.
Khothi lalikulu mdziko muno linaweruza kuti chisankho chamtsogoleri wadziko cha 2019 chichitikenso, chimodzimodzinso dziko la Kenya lomwe linaperekanso chigamulo chotere m’chaka cha 2017.