Mlembi Wamkulu watsopano wa chipani cha Malawi Congress(MCP), a Richard Chimwendo Banda, wati boma ladzipereka pokweza dera laku chigwa cha Shire komanso dziko lonse la Malawi.
A Chimwendo Banda anena izi pa msonkhano umene achititsa pa sitolo zapa Nchalo ku Chikwawa.
“Boma silikufuna anthu avutike ndi njala. Ichi ndi chifukwa chake boma likupereka chakudya kwa anthu omwe akuvutika ndi njala,” anatero a Chimwendo Banda, nkuonjezera kuti, “Kuphatikiza kugawa chakudya, boma likulimbikitsa anthu kuchita ulimi othilira pothana ndi njala.”
Iwo anati boma, motsogozedwa ndi Prezidenti Chakwera, likumanga misewu komanso njanji pofuna kulimbikitsa chitukuko ku Chikwawa ndiku Nsanje.
“Boma la Prezidenti Chakwera likumanga njanji yomwe ena anailephera pofuna kulumikiza chigwachi ndikumtunda. Kuphatikiza apa, boma lipaka phula nsewu wa Chapananga,” anafokoza chomwechi Mlembi Wamkulu watsopano wa MCP-yu.
Poyankhulanso pa msonkhanowo, Mneneri watsopano wa MCP, a Jessie Kabwila, analangiza anthu kufunika kodzaponya voti pa chisankho cha chaka cha mawa.
“Chonde ndikukupemphani kuti mukalembetse ndi kudzavotera boma lilipoli. Inu mukuona chitukuko chomwe bomali likuchita… njanji ku Nsanje, misewu yabwino m’madera osiyana-siyana ndi zinthu zina,” anapempha a Kabwila.
Iwo ananenetsa kuti pa chisankho cha chaka cha mawa, MCP idzapambana ndi mavoti oposa theka la mavoti onse.