Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Nkhani

MCP ipitiriza kukwaniritsa malonjezo — Kabwila

Chipani cha Malawi Congress (MCP) chati sichichita nawo ndale zoononga, zodana komanso zolozana zala ndipo m’malo mwake chipitiriza kugwira ntchito za chitukuko zolozeka zimene zitasinthe miyoyo ya anthu m’dziko muno.

Ofalitsankhani za chipanichi, a Jessie Kabwila, anena izi m’dera la T/A Masula ku Mitundu m’boma la Lilongwe kumene anakaona mmene ntchito yomanga nyumba ya atsikana achialubino a m’derali ikuyendera.

A Kabwila ati chipani chawo chikuyika pa mtima umoyo wa anthu m’dziko muno posatengera kusiyana ndipo apitiriza kukwaniritsa malonjezo amene anapereka kwa a Malawi.

Iwo ati MCP ipitiriza kugwira ntchito zachitukuko ndi kuzikwaniritsa kuti umoyo wa anthu achialubino usinthe powateteza, kuwapatsa mwayi  ndi kuwathandizira m’magawo osiyanasiyana.

M’modzi mwa atsikana amene awamagira nyumba, Siyana Kamumtengo, wathokoza boma powamangira nyumbayi ndipo wati tsopano sadzikhala mwa mantha.

Boma lamanga nyumba zoposa 65 za anthuwa ndipo mwa izo, 57 zatha kale.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Chakwera off to Zambia

Eunice Ndhlovu

Ochita malonda athandiza ana asukulu

Mayeso Chikhadzula

Kasiya Rutile, Graphite mining project promises long-term economic boost

Doreen Sonani
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.