Mtsogoleri wa mpingo wa Salvation for All Ministries International, Apostle Clifford Kawinga, wapereka K25 million kunyumba yosunga ana amasiye ya Home of Hope Orphanage m’boma la Mchinji ngati chikondwelero pa tsiku lawo lobadwa.
A Kawinga aperekanso matumba 100 a chimanga, matumba 20 a nyemba, matumba 10 a mpunga, mabulangeti 100, komanso makope kwa ana a pamalowa.
Mbali inayi, achikulire 1,000 ochokera m’madera ozungulira Home of Hope Orphanage, alandira shuga, mchere, mafuta ophikira komanso sopo, mwa zina zambiri.
Apostle Kawinga anati ang’ono awo awiri anakhalapo pa malowa ali achichepere kutsatira imfa ya abambo awo.
Reverend Thomson John Chipeta ndi amene anakhazikitsa malowa m’chaka cha 1998 ndi ndalama yokwana K100 ndipo anayamba ndi ana 20 koma pano pali ana oposa 760.