Mkulu wa Malawi Broadcasting Corporation (MBC), a George Kasakula, walengeza kuti tsopano nyumba yowulutsa mawuyi makanema ake a MBC TV komanso 2 on the Go asintha nambala za matchanelo amene amaoneka pa DSTV komanso GOTV.
A Kasakula ayankhula izi pa msonkhano wa olembankhani umene akonza limodzi ndi a Multi Choice Malawi munzinda wa Lilongwe.
Ikamafika nthawi ya 12 koloko komanso 1 koloko lero masana pa GOTV MBC TV 1 idzioneka pa nambala ya 15 ndipo MBC 2 on the Go idzioneka pa nambala 16.
Pomwe pa DSTV MBC 1 idzioneka pa nambala 268 ndipo MBC 2 on the go ikhala pa nambala 269.
A Kasakula ati MBC yachita izi pofuna kuonetsetsa kuti a Malawi akupeza uthenga komanso ma pologalamu ake mosavuta.