Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani Sports

MBC Socials yagonja 4-3 kwa Mablacks

Timu ya mpira wa miyendo ya anthu ogwira ntchito ku MBC yagonja ndi zigoli zinayi kwa zitatu pa masewero omwe inali nawo ndi akatswiri oyimba nyimbo za chamba cha Reggae omwe amakhala ku Chileka, a Black Missionaries, omwenso amadziwika kuti Mablacks.

Pa masewerowa omwe anachitikira pa bwalo la sukulu ya pulaimale ya Ngumbe m’boma la Blantyre, timu ya Mablacks ndi yomwe inayamba kutsogola pomwetsa zigoli zitatu inayo kwachilowere.

Ena mwa akatswiri a timuyi omwe anamwetsa zigoli ndi katswiri oyimba Keyboard, Chizondi Fumulani.

Koma olemba ndi kuwulutsa nkhaniwa anawonetsa chamuna mchigawo chachiwiri pomwetsa zigoli zitatu ndikupangitsa kuti masewerowa akhale 3-3.

Chakumapeto, a MBC Socials anawonetsa kutopa pang’ono, zimene zinapereka mpata kwa akatswiri oyimbawa kumwetsa chigoli chopambanira kuti masewero athere 4-3.

Polankhula pa mapeto a masewerowa, otsogolera timu ya MBC, Noel Chinkwende, wati akonzanso masewero ena achibwereza kuti adzabweze chipongwe.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

TIMASOWEKERA ZIPANGIZO ZOJAMBULIRA KANEMA

MBC Online

Mwaungulu tsopano adzivala Jersey 11

Romeo Umali

Atsiriza kufufuza za imfa ya anthu asanu ku Blantyre

Blessings Kanache
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.