Anthu ochita malonda ochokela ku Nsungwi ku Area 25 mu mzinda wa Lilongwe asonkhana panja pa bwalo la High Court kumene akuyembekezera kuti amve chigamulo pankhani ya m’mwenye wina amene adamusumira sabata zingapo zapitazo.
M’mwenyeyu dzina lake ndi Salahudding Akbar ndipo anthuwa amati iye ‘amatsitsa kwambiri mitengo ndi kuphangira pochita malonda’ pa shopu yake ndipo kenaka mmwenyeyo adakawasumira mlandu mavendawo.
Zimenezi zidachitika pamene unduna wa zamalonda utalamula Akbar kuti achoke pa msika wa Nsungwi pasanathe masiku khumi ndi anayi.
Akuunika mlanduwu ndi Justice Kenyatta Nyirenda ndipo sabata yathayi adaayimitsa kaye nkhaniyi ndi cholinga chakuti maloya ambali zonse ziwiri aunikire bwino kalata zofunika pa nkhaniyi.
Malipoti osatsimikizika akusonyeza kuti a Akbar asamutsa katundu wao yense usiku wapitawu.
#MBCDigital
#Manthu