Banja la bambo ndi mayi Loyd lathokoza chipatala cha boma cha Bwaila chimene chinathandiza mayi Loyd omwe anadwalako matenda a Kadzamkodzo.
Adindo apa chipatalachi adawapatsakonso uphungu komanso zipangizo zoyambira malonda.
Bambo Loyd ati atakumana ndi vutoli, anthu ena adawauza kuti awasiye akazi awo koma iwo adakana mpakana adapeza bwino ndipo chifukwa cha ichi iwo alimbikitsa mabanja ena kuti matendawa ndi ochizika.
Izi zikuchitika pa mwambo okumbukila ntchito yolimbana ndi nthendayi.