Mwambo oyankhula pa maliro a malemu Everes Kayanula uli mkati pa bwalo la masewero la Mdika m’mudzi mwa Mtsiro m’boma la Dowa.
Mfumu Mtsiro, Mfumu Simwira ndi oimira banja la Katsukunya ati malemu Kayanula anali mlangizi komanso mlerakhungwa kwa anthu ambiri.
Choncho akubanja komanso mafumu adandaula kaamba ka imfa yao.
Apa, mafumu apempha ana komanso anthu osala kuti azikumbuka kumudzi momwe malemu amachitira.
Malemu Kayanula asiya ana anayi.